Polisi ya Limbe yatsimikiza za imfa ya bamboo wa zaka 66 Davison Tambala yemwe wazipha yekha kudera la mfumu Chipagala ku BCA mu mzinda wa Blantyre.

Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Limbe Sub Inspector Sam Kadyole, thupi la bambo Tambala linapezedwa likulendewera kudenga la nyumba yawo madzulo a lachiwiri pa 17 June.

Sub Inspector Kadyole auza Eagle FM online kuti kafukufuku akadadali mkati pakadalipanno ofuna kupeza chomwe bamboyu wadziphera.

Iwo apempha mzika za dziko lino kumafunsila uphungu oyenera kunthambi ya Victim support unit yomwe imapezeka pa polisi iliyonse yomwe alinayo pafupi pamene akumana ndi mavuto osiyanasiyana m’malo mochotsa moyo wawo.

M’mawu ake mfumu Chipagala yati izi ndi zodandaulitsa kaamba koti akhala akulimbikitsa anthu awo kuti azitha kugawana ndi anzawo komanso atsogoleri amipingo zankhawa zomwe akukumana nazo pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Related posts

Polisi ya Limbe yati chiwerengero cha ngozi chatsika ndi 22 Percent.

Bambo wa zaka 62 wafa poziombera ndi mfuti mumzinda wa Blantyre.

Apolisi ku Limbe amanga bambo wazaka 24 kamba komanimiza anthu kuti ndi msilikali wa MDF