Polisi ya Limbe yati chiwelengero cha milandu chatsika ndi 15 % mutheka ya chaka chino.

Polisi ya Limbe yati chiwelengero cha milandu yomwe anthu akhala akupalamula chatsika ndi 15 % mutheka ya chaka chino.

Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Limbe Sub inspector Sam Kadyole, polisi yi yakwanitsa kuchepetsa chiwelengerochi pamene milandu yokwana 159 ndi yomwe polisiyi yalandira kuchokera mu January kufika June chaka chino kuyerekeza ndi milandu188 yomwe polisiyi inali italandira munyengo ngati yomweyi chaka chatha.

A Kadyole ati chiwelengerochi chatsika kutsatira ndondomeko zosiyanasiyana zomwe polisi yi inakhazikitsa pofuna kuthana ndi mchitidwe waumbava ndi umbanda kuderali.
Iwo anati mwa zina polisiyi yakhala ikugwira ntchito limodzi ndi atsogoleri akumadera komanso kudzalidwa kwa makanema achinsinsi mumsika wa Limbe zomwe zathandizira kuti ntchito yogwira anthu umbava ndi umbanda ikhale yosavuta.

Related posts

Government announces resumption issuance and printing of passport services

Atsogoleri akumadera alimbikitsa abambo kukhala patsogolo pokhazikitsa magulu owathandizira kumapeza ndikusunga ndalama pofuna kuchepetsa chiwelengero cha abambo odzipha okha mdziko muno.