Police ya Limbe yapempha anthu okhala kumadera omwe alipansi pa polisiyi kukhala atcheru pamene akhristu akukonzekera nyengo ya Pasaka yomwe ndi nthawi yokumbukira mazunzo, imfa komanso kuuka kwa Yesu khristu.

Mneneri wa polisi ya Limbe.

Mu nyengoyi akhristu amipingo yosiyanasiyana amakonza zochitika monga njira ya mtanda, ulendo wa ndawala, Tsiku la Kanjedza komanso misonkhano yolamilikira kumadera osiyanasiyana. 

M’neneri wa polisi ya Limbe Sergeant Aubrey Singanyama wati pamene akhristu akukumbukira nyengoyi akubanso nawo amapezelapo mwayi ochita zaupandu.

Sergeant Singanyama wati monga mwa udindo wawo oteteza miyoyo ndi katundu wa anthu, apolisi alimbikitsa njira zingapo monga kukhazikitsa zipata zapamsewu komanso ntchito yoyendera madera osiyanasiyana omwe ali pansi pa polisiyi.

Iwo apitiriza kukumbutsa anthuwa za udindo waukulu omwe ali nawo pawokha posamalira ndi kuteteza katundu wawo ndi kupewa kuyenda nthawi yolakwika mwa zina.

Related posts

Atsogoleri akhale patsogolo popeza mayankho othana ndi mavuto omwe akuta dziko lino-Sadana