Phungu yemwe akuyimira kudela la Blantyre-Chichiri-Misesa walonjeza zitukuko kudelali akazapambana chisankho mwezi wa September

Yemwe akuimira pampando wa phungu wanyumba yamalamulo kudera la Blantyre-Chichiri-Misesa Themba Mkandawire wayamba ntchito yokambirana ndi mafumu pazina mwa zitukuko zomwe akufuna kuchita pamene chisankho chapa 16 September chikuwandikira.

A Mkandawire omwe anapambana pazisankho zachipulula posachedwapa mchipani cha Democratic Progressive-DPP ati cholinga cha mikumanoyi ndi kufuna kukhazikitsa ubale wabwino pakati pawo ndi mafumu omwe amayang’anira anthu akudera.

Iwo ati mikumanoyi ithandizira kupititsa patsogolo ntchito zachitukuko kuderali lomwe kwa nthawi yaitali lakhala lili lotsalira pankhani yachitukuko.

Zina mwa zitukuko zomwe a Mkandawire ati akufuna kuchita kuderali ndi kuphatikizirapo kupaka phula msewu wa Limbe-Manje, kubweretsa magetsi kudera ka mfumu Mtambo komanso ntchito yokuza chipatala cha Limbe.

Picture: Kingsley Sowa

Related posts