Phungu wa dera la kum’mwera cha ku m’mawa kwa mzinda wa Blantyre Sameer Suleiman apambana pachisankho chachipulula atogonjeza a Wild Ndipo yemwe ndi mfumu yakale ya mzinda wa Blantyre

Phungu wanyumba yamalamulo kudera la Kum’mwera- chakum’mawa Kwa mzinda wa Blantyre a Sameer Suleiman apambana pachisankho chachipululala chomwe chachitika kuderali lachiwiri.

A Suleiman apambana pachisankhochi ndi mavoti 458 pamene yemwe amapikisana nawo a Wild Ndipo apeza mavoti 17.

Izi zikutanthauza kuti a Suleiman ndi omwe adzaimire pampando waphungu wanyumba yamalamulo pachipani Cha DPP kudera la Chigumula-BCA -Club Banana pachisankhochi chapa 16 September Chaka chino.

Related posts