Mfumu yaikulu Kapeni ya mumzinda wa Blantyre yati ntchito yozindikiritsa anthu za nkhani ya chitukuko ndi yofunika kwambiri polimbikitsa a Malawi kutenga nawo mbali pantchitozi ndicholinga chofikira masomphenya a chaka cha 2063.
Izi zayankhulidwa pomwe unduna oona kuti pali kusasiyana pantchito pakati pa amayi ndi abambo ukugwiritsa ntchito mwezi uno wa May kulimbikitsa anthu kutenga nawo mbali pa ntchito zachitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika m’madera mwawo.
Poyankhula ndi Eagle FM Mfumu yaikulu Kapeni yayamikira mzika zina zakudera zomwe zikugwira ntchito yotukula madera awo pomanga midadada ya sukulu, milatho komanso kukonzanso miseu.
Apa mfumuyi yapempha boma ndi magulu ena okhudzidwa kufikira madera osiyanasiyana a mumzinda wa Blantyre ndi maboma ena m’dziko muno ndi mauthenga okhudza kufunika kotenga nawo mbali pantchito zachitukuko.
Iwo alangizanso mafumu ena pamodzi ndi anthu awo kuti asinthe kaganizidwe ndi kusiya kudalira boma pantchito iliyonse yokhudza chitukuko.
Photo Credit: Internet