Home National Mfumu Kapeni yalimbikitsa chitukuko mu mzinda wa Blantyre pofuna kufikira maloto a chaka cha 2063

Mfumu Kapeni yalimbikitsa chitukuko mu mzinda wa Blantyre pofuna kufikira maloto a chaka cha 2063

by Kingsley Sowa
0 comments

Mfumu yaikulu Kapeni ya mumzinda wa Blantyre yati ntchito yozindikiritsa anthu za nkhani ya chitukuko ndi yofunika kwambiri polimbikitsa a Malawi kutenga nawo mbali pantchitozi ndicholinga chofikira masomphenya a chaka cha 2063.

Izi zayankhulidwa pomwe unduna oona kuti pali kusasiyana pantchito pakati pa amayi ndi abambo ukugwiritsa ntchito mwezi uno wa May kulimbikitsa anthu kutenga nawo mbali pa ntchito zachitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika m’madera mwawo.

Poyankhula ndi Eagle FM Mfumu yaikulu Kapeni yayamikira mzika zina zakudera zomwe zikugwira ntchito yotukula madera awo pomanga midadada ya sukulu, milatho komanso kukonzanso miseu.

Apa mfumuyi yapempha boma ndi magulu ena okhudzidwa kufikira madera osiyanasiyana a mumzinda wa Blantyre ndi maboma ena m’dziko muno ndi mauthenga okhudza kufunika kotenga nawo mbali pantchito zachitukuko.

Iwo alangizanso mafumu ena pamodzi ndi anthu awo kuti asinthe kaganizidwe ndi kusiya kudalira boma pantchito iliyonse yokhudza chitukuko.

Photo Credit: Internet

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00

Connection Information

To perform the requested action, WordPress needs to access your web server. Please enter your FTP credentials to proceed. If you do not remember your credentials, you should contact your web host.

Connection Type