Apolisi ku Limbe amanga bambo wazaka 24 kamba komanimiza anthu kuti ndi msilikali wa MDF

Apolisi ku Limbe akusunga mchitolokosi cha apolisi bambo wazaka 24 Emmanuel Davie pomuganizira kuti amanamiza anthu kuti ndi msilikali wa Malawi Defense Force- MDF.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Limbe Sub-inspector Chibisa Mulimbika, bamboo oganizilidwayu wakhala akubela ndalama kwa anthu ochokera kudera la Bangwe.

A Mulimbika awuza eagle online kuti oganizilidwayu amavala unifolomu yachisilikali ndipo anaonedwa kudera la Chipagala komwe amabela anthu ndalama powanamiza kuti awalemba ntchito kunthambi ya asilikali mtsogolo muno.

Sub Inspector Mulimbika anati anthuwa anakaneneza bamboo oganizilidwayu kupolisi ya Bangwe komwe apolisi ofufuza anakwanitsa kumanga mkuluyu kutsatira kafukufuku yemwe anachita kuphatikizirapo kunthambi ya Asilikali ya MDF komwe anatsikimiza kuti mbamboyu samagwira ntchito kunthambiyi.

Picture: Sub inspector Chibisa Mulimbika

Related posts

Polisi ya Limbe yati chiwerengero cha ngozi chatsika ndi 22 Percent.

Bambo wa zaka 62 wafa poziombera ndi mfuti mumzinda wa Blantyre.

Polisi ya Limbe yatsimikiza za imfa ya bamboo wa zaka 66 Davison Tambala yemwe wazipha yekha kudera la mfumu Chipagala ku BCA mu mzinda wa Blantyre.