Khansala wadera la Chigumula a Wild Ndipo omwe anagonja pachisankho chachipulula kwa a Sameer Suleiman pachipani cha Democratic progressive-DPP ati ayimila derali ngati phungu oyima payekha pachisankho chapa 16 September.

A Ndipo awuza Eagle FM Online kuti pakadalipano alimbikitsa zokonzekera zawo zofuna kuimila ngati phungu wadera la Chigumula-BCA-Club Banana.

Iwo ati chidwi choimila ngati phungu oyima payekha kuderali chadza kutsatira mavuto ochuluka omwe analipo panthawi yachisankho chachipululachi.

A Ndipo ati ndi odzipereka kugwira ntchito yotukula derali akadzapambana pachisankho chomwe chikuyembekezera kuchitika pa 16 September.

‘Poyambira ndili napo kale kaamba koti kufikira pakadalipano ndine khansala wadera la Chigumula ndipo chikhulupiliro ndili nacho kuti chimene Mulungu anandilembera chichitika basi’, anatero Ndipo.

Panthawi yachisankho chachipulula chomwe chinachitika mwezi wa April chaka chino mumzinda wa Blantyre a Ndipo anagonja atapeza mavoti 17 kwa omwe amapikisana nawo a Sameer Suleiman anapeza mavoti 458.

Related posts