Tikufuna kukhazikitsa gulu lina lothanzira anthu odwala nthenda ya khansa ku Blantyre-Cancer Survivors Quest

Bungwe loyang’anira anthu omwe anapulumuka kunthenda ya khansa la Cancer survivors Quest lati likukonza zogwira ntchito yozindikilitsa anthu komanso kukhazikitsa gulu la anthu othandizira bungweli kudera la Chikuli mumzinda wa Blantyre.

Malingana ndi mkulu wabungwe la Cancer Survivors Quest a Chikhulupiliro Ng’ombe, bungweli likuyembekezera kugwira ntchitoyi kuyambira pa 10 mpaka pa 13 June chaka chino.

A Ng’ombe ati bungweli lakonza mwambowu kudera la Chikuli poganizira kuti derali ndilotentha kwambiri ndipo pali kuthekera koti dzuwa lamphamvu lomwe limaomba kuderali ndilomwe lachititsa kuti anthu ena apezeke ndi matendawa.

Iwo atinso bungweli likukonza zolimbikitsa anthu akudera komanso mafumu zaudindo omwe alinawo pozindikiritsa anthu ena zanjira zopewera nthendayi.

A Ng’ombe ati akuyembekezeranso kupeza ndalama zokwana K130, 000 zothandizira pa ntchitoyi.