Polisi ya Limbe yati chiwelengero cha ngozi zapamsewu chatsika ndi 22 pelesenti m’miyezi isanu ndi umodzi ya chaka chino kuyerekeza ndi nyengo ngati yomweyi chaka chatha.
Izi zadziwika pa mkumano wa komiti yaikulu pa polisiyi omwe unachitikira ku Nkhwazi Lodge ku Chigumula mumzinda wa Blantyre.
Mkulu wa polisi ya Limbe a Edwin Mnkhambo ati kutsika kwa chiwelengerochi kukutsatira njira zomwe polisiyi yakhala ikulimbikitsa pofuna kuchepetsa ngozi zamtunduwu.
Mwazina iwo ati kukhazikitsa malo ochuluka ochitira zipikisheni m’misewu yosiyanasiyana omwe polisiyi imayang’anira ndi zina mwa zomwe zathandizira kwambiri kuchepetsa chiwelengerochi.
Koma a Mnkhambo ati chiwelengero cha milandu yomwe anthu amapalamula kuphatikizirapo milandu yokuba chakwera ndi 3.7 pelesenti kuyerekeza ndi nyengo ngati yomweyi chaka chatha.
Iwo anapitilira kutsikimizira anthu okhala madera ozungulira polisiyi kuti apitilira kugwira ntchito ndi magulu osiyanasiyana poteteza miyoyo ya anthuwa komanso kuchepetsa chiwelengero cha ngozi za pamsewu.
Kumbali yake wapampando wa komiti yaikuluyi Abdul-Hamid Khan anati mkumanowu unali ofunikira maka pankhani yokhwimitsa chitetezo cha anthu okhala kuderali.