NICE Trust yalimbikitsa onse oyenera kuvota pachisankho kutenga gawo pakampeni yotsikimizira maina mukaundula wachisankho.

Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana mdziko muno la NICE Trust lalimbikitsa anthu omwe ali oyenera kuponya voti pachisankho chachaka chino kuti atenge mbali pantchito yotsikimizira maina mukaundula wachisankho.

Mkulu oyendetsa ntchito zabungwe la NICE Trust mumzinda wa Blantyre Mayi Glory Ngosi Maulidi ayankhula izi pamene bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC likuyembekezera kuchititsa ntchito yotsikimizira mainawa mumzinda wa Blantyre kuyambira pa 21 kufikira pa 23 May.

Mayi Maulidi ati pakadalipano bungweli lalimbikitsa ntchito yophunzitsa anthu zaubwino otenga nawo gawo pantchitoyi ngati mbali imodzi yokonzekera chisankho chapa 16 September.

Iwo alimbikitsanso anthuwa kugwiritsa ntchito ndondomeko yotsikimizira mainawa kudzera pa lamya za m’manja poimba *2509# yomwe ndi njira yothandizira kuchepetsa nthawi yomwe anthu angakhale pamzere kumalo omwe akhazikitsidwe ndi bungweli.

Bungwe la MEC likuyembekezera kuchititsa ntchitoyi m’magawo atatu pamene gawo loyamba lichitika pa 13 mpaka pa 15 May, gawo lachiwiri kuyambira pa 21 mpaka pa 23 May ndipo gawo lomaliza lichitika pa 29 mpaka pa 31 May chaka chino.

Related posts

1 comment

Masteni May 7, 2025 - 2:12 pm
Great
Add Comment