Lachiwiri pa 17 June, Bungweli laphunzitsa abusa komanso atsogoleri amipingo makumi awiri ochokera mipingo yosiyanasiyana omwe ali pansi pagulu la Leyman Pastors Fraternal.
Poyankhula ndi Eagle FM Online, mkulu wa bungwe la Chiyembekezo Center for transformation Bishop Patrick Mbewe anati atsogoleri amipingo ochuluka akulephera kugwira ntchito yawo bwino lomwe kaamba ka mavuto azachuma zomwe zachititsa kuti bungweli likhazikitse ntchitoyi.
A Mbewe anati mwa zina, atumiki komanso atsogoleri amipingowa alimbikitsidwa kuti akhoza kumapanga fetereza komanso manyowa pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka m’madera mwawo zomwe ndi zothandizira kusunga chonde munthaka komanso kuchepetsa ndalama zomwe angagwiritse ntchito kukagula fetereza pamsika yemwe ndi okwera mtengo pakadalipano.
Wapampando wagulu la Leyman Pastors Fraternal Bishop Kenneth Chikopa wati maphunzirowa abwera panthawi yake poganizira zakukwera kwa mitengo ya fetereza pamsika.
A Chikopa anati gululi lionetsetsa kuti lagwiritsa bwino ntchito upangili omwe awupeza pamaphunzirowa pokweza umoyo wawo ngakhalenso madera omwe akuchokera.