Malinga ndi a Nkuzi Banda a Malawi akupitilira kukumana ndi mavuto osiyanasiyana monga vuto la njala, kusowa kwa mafuta agalimoto komanso kukwera kwa mitengo yakatundu pamsika zomwe zikupsinja umoyo wa mzika zadziko linozi.
Iwo anati mwazina dziko lino lili ndi zipangizo zokwanira monga Nyanja ya Malawi, Mtsinje wa Shire zomwe zingathandizire dziko lino kumakolola chakudya chokwanira ngati boma lingagwiritse ntchito moyenera zipangizozi polimbikitsa ulimi wanthilira komanso ntchito zamigodi zomwe zili ndikuthekera kothandizira dziko lino kumapeza ndalama zakunja.
A Banda anati izi ndi zina mwa zomwe chipani chawo chikuyembekezera kulimbikitsa chikadzapambana pachisankho chapa 16 September.
Iwo anapitilira kunena kuti pakadalipano akukonza dongosolo lolembetsa chipanichi pofika sabata yamawa.