Bambo wa zaka 62 wafa poziombera ndi mfuti mumzinda wa Blantyre.

Bambo wa zaka 62, Frank Kayuni wafa ataziombela ndi mfuti m’mawa wa lachiwiri pa 15 July pachipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre pomwe amalandira thandizo la mankhwala.

Malinga ndi malipoti mkazi wa bamboyu anamva kulira kwa komanso kukuwa kwa bambowa kuchokera kuchipinda ndipo atathamangila kuchipindachi iwo anapeza bambo yu ali chikomokere.

Mothandizana ndi akubanja, iwo anathamangira nawo kuchipatala bambowa komwe amwalira akulandira thandizo la mankhwala.

Thupi la malemuwa analitengera kuchipatala cha Queen Elizabeth Central komwe achipatala anatsimikiza kuti bambowa amwalira kamba ka bala lamfuti pachifuwa.

Padakali pano apolisi akufufuzabe chifukwa chomwe malemuwa achitira izi.

Malemu Frank Kayuni amachokera m’mudzi mwa Chizali kwa mfumu yaikulu Mwalambia m’boma la Chitipa.

Related posts

Polisi ya Limbe yati chiwerengero cha ngozi chatsika ndi 22 Percent.

Polisi ya Limbe yatsimikiza za imfa ya bamboo wa zaka 66 Davison Tambala yemwe wazipha yekha kudera la mfumu Chipagala ku BCA mu mzinda wa Blantyre.

Apolisi ku Limbe amanga bambo wazaka 24 kamba komanimiza anthu kuti ndi msilikali wa MDF