Atsogoleri omwe akuimira kudera Blantyre-Chichiri -Misesa agwirizana zochita misonkhano yamtendere.

Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana mdziko muno la NICE-TRUST lalangiza mzika zadziko lino kuvotera atsogoleri okhawo omwe ali ndi masomphenya otukula madera awo.

Izi zayankhulidwa pamtsutso wa atsogoleri andale omwe unachitikira pa sukulu ya pulaimale ya Kapeni demonstration kudera la Soche mumzinda wa Blantyre.

Mtsutsowu unakonzedwa pofuna kupereka danga kwa atsogoleri omwe akuimira pachisankho chikubwerachi kudera la Blantyre-Chichiri-Misesa kufotokozera anthu akudera lawo zina mwa mfundo zachitukuko zomwe akonzera anthu akuderali atapambana pachisankho chapa 16 September.

Poyankhula pakutha pa mtsutsowu mkulu oyendesa ntchito za Nice trust ku Blantyre mayi Glory Ngosi Maulidi apempha anthu kutenga nawo gawo pamisonkhano yazipani zosiyanasiyana komanso oyima paokha kuti athe kupanga chiganizo choyenera posankha adindo omwe ali ndi masomphenya otukula dela lawo.

M’modzi mwa anthu akuyimila ngati phungu kudelali pansi pa chipani cha DPP Themba Nkandawire anayamikira bungwe la Nice kamba kamsonkhanowu komanso kulimbikitsa ntendere nthawi ino yamisonkhano yokopa anthu.

Nkandawire anati nthawi yakwana tsopano kuti oyimira pamipando yosiyanasiyana atsindike potsitsa mfundo m’malo monyozana wina ndi nzake.

Pogwirizana ndi a Nkandawire yemwe akuyimira ngati phungu ku delali pansi pa chipani cha UDF Illy Majawa Mombera wati ndiozipereka kutukula delali akazapambana pachisankho chapa 16 September.

Mtsutsowu unabweretsa pamodzi anthu omwe aonetsa chidwi choimira kudelali pa mpando wa ukhansala komanso phungu wa nyumba yamalamulo monga, Lous Ngalande, Paul Kachitsa, Themba Nkandawire komanso Illy majawa Mombera mwa ena.

Kupatula ku Blantyre-chichiri-Misesa bungwe la Nice Trust lachititsa mtsutso ngati omwewu kudela la Ndirande-malabada komanso kudela lapakati mundzinda wa Blantyre.

Related posts