Mfumu Solomon yakudera la Mfumu yaikulu Bvumbwe m’boma la Thyolo yayankhula izi kutsatira kukhazikitsidwa kwa gulu lomwe akulitchula kuti Umodzi wa abambo m’bomali.
Mfumu Solomon yati gululi lomwe linayamba mchaka cha 2015 lathandizira kutukula dera lake pamene mawanja ochuluka tsopano akutha kuchita ntchito zamalonda zosiyanasiyana komanso ulimi waziweto.
A Solomon ati kuyerekeza ndi mbuyomu, chiwelengero cha abambo odzipha okha kuderali chachepa pamene abambo akutha kumakambirana momasuka nkhani zosiyanasiyana zomwe zimakhudza umoyo wawo.
Kumbali yake, Mlembi wagulu la Umodzi wa abambo a Samuel Mpola ati abambo amakumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizirapo mavuto azachuma omwe akhala akuthandizira kukwera kwa chiwelengerochi.
A Mpola apempha mabungwe opereka ngongole kuphatikizirapo bungwe la NEEF kuthandizira magulu monga awa ndicholinga chokwaniritsa masomphenya otukula abambowa.
Gululi linayamba mchaka cha 2015 ndi mamembala asanu ndi anayi ndipo pakadalipano lili ndi mamembala oposera makumi anayi-40.