Atsogoleri akhale patsogolo popeza mayankho othana ndi mavuto omwe akuta dziko lino-Sadana

Yemwe akuimira pa mpando wa khansala woima payekha kudera la BCA-Chigumula mumzinda wa Blantyre a Sadana Bakili atsindika kufunika koti atsogoleri azitengapo gawo lalikulu pothana ndi mavuto omwe mzika zakumadera zikukumana nawo.

A Bakili ayankhula izi lachitatu pa 4 June pomwe amayendera ndi kuchezera anthu odwala komanso achikulire ku dera la mfumu Chipagala ku BCA mu mzinda Blantyre.

Poyankhula ndi wailesi ino a Bakili anati kupatula kuyendera ndi kuthandiza anthu achikulire, derali likusowekera ntchito zachitukuko monga madzi aukhondo ndi kulimbikitsa ntchito zotukula amayi ndi achinyamata zomwe ati adzalimbikitsa akazapambana pachisankho chapa 16 September.

Iwo atsindikanso kufunika kosintha kaganizidwe pakati pa atsogoleri a m’madera poonetsetsa kuti mzika zakudera zikutha kukhala ndi zochita zowathandizira kupeza ndalama m’malo mogwiritsidwa ntchito ndi andale poyambitsa ziwawa pomwe dziko lino likuwandikira kuchisankho.

Related posts

Youths urged to be patriots of their communities