A Enala Yesaya achipani cha MCP apambana pazisankho zachipulula za aphungu kudera la Blantyre-Chichiri-Misesa.

Yemwe akuimila paudindo waphungu kudera Blantyre-Chichiri-Misesa muchipani cha Malawi congress-MCP Enala Yesaya wapambana pachisankho chachipulula chomwe chachitika lachitatu pasukulu ya pulaimale ya Kanjedza.

A Yesaya apambana pachisankhochi ndi mavoti 287 kugonjetsa a Charles Mwambyale omwe apeza mavoti 45.

Iwo ati ndiwokondwa ndi kupambanaku ponena kuti kukutanthauza chikhulupiliro chomwe anthu akuderali alinacho pokweza amayi paudindo.

A Yesaya alimbikitsa anthu akuderali kuti apitilire kukhala pambuyo pawo mpaka patsiku lachisankho pomwe ati ndi wodzipereka kutukula derali.

Kumbali yake wachiwiri kwa mkulu wa achinyamata muchipani cha MCP a Isaac Ramsey Khan anati chisankhochi chayenda bwino ndipo ayamikila anthu otsatira chipanichi potsatira ndondomeko za demokalase posankha munthu wamkazi paudindowu.

Related posts