Gulu la mzika zokhudzidwa la union of concerned citizens’ lalimbikitsa a Malawi kukhala a mtendere pamene tsiku loponya voti likuwandikila.
Izi zayankhulidwa lachinayi pamsokhano wa olembankhani omwe unachitika munzinda wa Blantyre.
M’Modzi mwa mamembala a gululi a Edwards Kambanje ati Malawi likadali dziko loopa Mulungu choncho nyengo ya misonkhano yokopa anthu isakhale nyengo yogawanikana pakati pa a Malawi ngakhale akusiyana zipani zotsatira.
A Kambanje ati gululi lipitiliza kufalitsa mauthenga okhudza mtendere ndi kulolelana pakati pa a Malawi zomwe ndi zofunika mu ulamuliro wa demokalase.