by Kingsley Sowa
0 comments

Anthu ena okhala kudera la Machinjiri mumzinda wa Blantyre adzudzula akuluakulu polephera kuchitapo kanthu kwa anthu omwe akukozera nyumba zawo.

Eagle FM online itafika kumalowa inapeza kuti anthu ochuluka omwe akuchita malonda maka ogulitsa mowa akumakozera pakhoma la nyumbayi zomwe zikuchititsa kuti pamalowa pazituluka fungo loipa kufikira poti imodzi mwa nyumba yomwe ili pamalowa ili pachiopsezo chokugwa.

Poyankhula ndi Eagle FM online m’modzi mwa anthu omwe akhudzidwa ndi vutoli Andrew Manyera anati kwa nthawi yaitali akhala akudandaulira adindo koma mpaka pano palibe chomwe chikuchitika kotero apempha mbali zokhudzidwa kuti zilowererepo ndikupeza njira zothetsera vutoli ponena kuti sangakwanitse kukonzanso nyumba yawo kutsatira mavuto a zachuma omwe iwo akukumana nawo pakadalipano. 

Poyankhulapo pa nkhaniyi m’modzi mwa ma membala a komiti yoyang’anira msika wa Chikapa a Hapin Songa avomereza kuti vutoli akulidziwa Ndipo apempha mbali zonse ziwiri kuti zigwilane manja pofuna kuthetsa kusamvana kwao pokonza ngalande ngati njira imodzi yofuna kuteteza nyumbayi.

A Songa ati kusagwira bwino ntchito kwa zimbudzi zomwe zili pa msikawu ndikomwe kukukhudza kwambiri ntchito za malonda pa malowa kamba koti khonsolo ya mzinda wa Blantyre ikulephera kulumikizitsa madzi ku zimbudzi zitatu zomwe zangomangidwa kumene pa msikawu

Mfumu Chilembwe ya mderali yati ikukonza zokumana ndi eni malo omwera mowa pa msikawu pofuna kuthetsa vutoli lomwe likuika pa chiopsezo chakufala kwa matenda odza kaamba kakusowa kwa ukhondo monga nthenda ya kolera.

Nkhani ya Andrew Manyera ndi imodzi mwa nkhani zomwe zikuulula zakukula kwa mchitidwe wa anthu ena okoza paliponse makamaka m’mizinda ya dziko lino ndipo ili ndi chenjezo kwa adindo kuchitapo kanthu pofuna kuthana ndi mchitidwewu.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00

Connection Information

To perform the requested action, WordPress needs to access your web server. Please enter your FTP credentials to proceed. If you do not remember your credentials, you should contact your web host.

Connection Type