Home National Ngati njira imodzi yoonetsetsa kuti atsogoleri amipingo maka akumadera akumidzi ali ndi chokudya chokwanira, bungwe la Chiyembekezo center for transformation lalimbikitsa ntchito yophunzitsa abusa komanso atsogoleri amipingo zamomwe angapangile feteleza pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka m’madera mwawo m’boma la Phalombe.

Ngati njira imodzi yoonetsetsa kuti atsogoleri amipingo maka akumadera akumidzi ali ndi chokudya chokwanira, bungwe la Chiyembekezo center for transformation lalimbikitsa ntchito yophunzitsa abusa komanso atsogoleri amipingo zamomwe angapangile feteleza pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka m’madera mwawo m’boma la Phalombe.

by Kingsley Sowa
0 comments

Lachiwiri pa 17 June, Bungweli laphunzitsa abusa komanso atsogoleri amipingo makumi awiri ochokera mipingo yosiyanasiyana omwe ali pansi pagulu la Leyman Pastors Fraternal.

Poyankhula ndi Eagle FM Online, mkulu wa bungwe la Chiyembekezo Center for transformation Bishop Patrick Mbewe anati atsogoleri amipingo ochuluka akulephera kugwira ntchito yawo bwino lomwe kaamba ka mavuto azachuma zomwe zachititsa kuti bungweli likhazikitse ntchitoyi.

A Mbewe anati mwa zina, atumiki komanso atsogoleri amipingowa alimbikitsidwa kuti akhoza kumapanga fetereza komanso manyowa pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka m’madera mwawo zomwe ndi zothandizira kusunga chonde munthaka komanso kuchepetsa ndalama zomwe angagwiritse ntchito kukagula fetereza pamsika yemwe ndi okwera mtengo pakadalipano.

Wapampando wagulu la Leyman Pastors Fraternal Bishop Kenneth Chikopa wati maphunzirowa abwera panthawi yake poganizira zakukwera kwa mitengo ya fetereza pamsika.

A Chikopa anati gululi lionetsetsa kuti lagwiritsa bwino ntchito upangili omwe awupeza pamaphunzirowa pokweza umoyo wawo ngakhalenso madera omwe akuchokera.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00

Connection Information

To perform the requested action, WordPress needs to access your web server. Please enter your FTP credentials to proceed. If you do not remember your credentials, you should contact your web host.

Connection Type