Gulu la ophunzira omwe anaphunzira pasukulu ya sekondale ya Mulanje muzaka zapakati pa 2008 ndi 2011 lati likukonza zopeza njira zosiyanasiyana zopezera ndalama zothandizira kuchepetsa ena mwa mavuto omwe sukuluyi ikukumana nawo.
Mneneri wa gululi Azeez Losa ndiye wayankhula izi pamene gululi likukonza zokhala ndi mkumano omwe uchitike pa 7 July chaka chino ku Saiwa garden ku Njamba mumzinda wa Blantyre.
Losa wati mwa zina, gululi likuyembekezera kukambirana zanjira zopezera chuma komanso kugawana mfundo zochitila malonda ndicholinga chopeza ndalama zomwe zithandizire kulipilira sukulu fees kwa ophunzira osowa komanso kugula zipangizo zophunzilira pasukuluyi.
Iwo anapitilira kunena kuti ngati njira imodzi yokwezera kakhozedwe ka ophunzira pasukuluyi, gululi likukonza zolimbikitsa ndondomeko younikila ophunzira pa ntchito zomwe akufuna kudzagwira akazamaliza maphunziro awo.
Apa Losa wapempha ophunzira onse omwe anaphunzira pasukulu yi ndipo akukhala mdziko muno komanso maiko ena kuthandizirapo pantchitoyi ndi cholinga choti ifikire ophunzira ochuluka.