Bungwe loyang’anira masewero achisodzera mdziko muno lati likukonza zochititsa ntchito yotsikimiza zaka za osewera league yachaka chino isanayambe.
Mlembi wamkulu wabungweli Rabson Wood-well wayankhula izi pofotokozera wailesi ino zamasiku omwe bungweli likuyembekezera kutsegulira mpikisano wachaka chino.
Poyankhula ndi Eagle FM Wood-well wati pali zifukwa zingapo zomwe akuunikila mpikisano wachaka chino usanayambe monga kuchita mkumano ndi banki ya First Capital yomwe imathandizira mpikisanowu komanso bungwe loyendetsa masewero ampira wamiyendo mdziko muno la FAM.
Iye anati ndalama zikapezeka, bungweli likuyembekezera kutsegulira mpikisano wachaka chino wa osewera osapitilira zaka makumi awiri pa 31 May pomwe mipikisano ina ikuyembekezera kuyamba kumayambiliro kwa mwezi wa June.
Photo Credit: Internet