Mtsogoleri wachipani cha Malawi congress Dr. Lazarus Mccarthy Chakwera avomereza kugonja pachisankho chomwe chinachitika pa 16 September chaka chino.

Dr. Chakwera avomereza kugonja kwawo pamene amayankhula ku mtundu wa a Malawi ku nyumba ya boma mumzinda wa Lilongwe masana a lachitatu.

Dr. Chakwera ati achita izi pofuna kulemekeza chifuniro cha a Malawi povotera Professor Arthur Peter Mutharika achipani cha Democratic Progressive-DPP ngati mtsogoleri wadziko lino pachisankhochi.

Iwo atinso achita izi ngati njira imodzi yolimbikitsira bata ndi mtendere pakati pa a Malawi zomwenso ndi ngodya za demokalase.

Komabe a Chakwera apempha bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC kufotokozera bwino a Malawi ena mwa madandaulo omwe zipani zandale kuphatikizirapo chipani cha Malawi Congress zinapereka pa zotsatira zachisankho.

Pomaliza iwo ati ndi okonzeka kugwira ntchito limodzi ndi a Mutharika ndicholinga chopititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.

Bungwe loyendetsa chisankho la MEC likuyembekezera kulengeza zotsatira zachisankho cha mtsogoleri wadziko lino nthawi ya 2 koloko masanawu.

Related posts