Yemwe akuima payekha pampando wa phungu kudera la Blantyre-Chichiri-Misesa a Paul Kachitsa adzudzula mchitidwe wa andale ena opereka katundu kwa anthu ovota munyengo ino ya misonkhano yokopa anthu.

A Kachitsa ayankhula izi lachisanu pomwe amayankhula kugulu la anthu omwe anasonkhana kudera la Quarry mumzinda wa Blantyre.

Poyankhula pamsonkhanowu a Kachitsa analonjeza zolimbikitsa ntchito zachitukuko zogwirika kuderali popereka zitsanzo za chitukuko chomanga midadada yasukulu kudera la Mtambo ndi kumanga milatho yolumikiza madera a Chigumula ndi Soche yomwe ikadalimkati pakadalipano.

A Kachitsa ati ayika chidwi chawo chachikulu pamisonkhano yolankhula mfundo zachitukuko zomwe akufuna kudzachita akadzapambana pachisankhochi ndipo alangiza anzawo omwe akupikisana nawo kuderali kupewa mchitidwe opereka katundu kwa anthu munyengoyi.

Ena mwa anthu omwe akupikisana kuderali ndi a Illy Majawa Mombera achipani cha United Democratic front, a Enala Shaba achipani cha Malawi Congress, a Themba Mkandawire achipani cha Democratic Progressive komanso a Louis Ngalande oyima pawokha mwa ena.

Related posts

Opposition Democratic progressive party again promise to bail out Malawians from challenges rocking the country.