Amalawi apewe ziwawa nyengo ya misonkhano yokopa anthu-NICE Public Trust

Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la NICE Trust lakumbutsa anthu omwe aonetsa chidwi choimila pachisankho chapa 16 September kulimbiikitsa mtendere pamene nyengo yamisonkhano yokopa anthu ikhale ikutsegulilidwa posachedwapa.

Izi zayankhulidwa lachinai pamkumano omwe bungwe la NICE Trust ndi bungwe la Anti-corruption bureau linakonzera anthu omwe awonetsa chidwi choimira paudindo wa phungu komanso khansala kudera la pakati mu mzinda wa Blantyre pamwambo omwe unachitikira pa sukulu ya pulaimale ya Dziwe.

Poyankhula pamwambowu mkulu oyang’anira ntchito zabungwe la NICE public trust mumzinda wa Blantyre Mayi Glory Ngosi Maulidi ati mkumanowu unapereka danga kwa omwe akufuna kuyimira pachisankhochi kufotokozera zina mwa ntchito za chitukuko zomwe azachite kuderali atapambana pachisankho chapa 16 September.

Mayi Maulidi ati nthawi yakwana tsopano kuti adindo azichita ndale zotsitsa mfundo m’malo mochita ndale zonyozana munyengo yamisonkhano yokopa anthu.

Kumbali yake mkulu ophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana ku Bungwe lothana ndi ziphuphu ndi katangale la Anti-corruption bureau a Jonathan Chisale adzudzula mchitidwe ogawa katundu kwa anthu munnyengo ya misonkhanoyi ponena kuti izi ndi zoletsedwa ndi malamulo achisankho.

Pamkumanowu bungwe la Nice trust linasanila mgwirizano ndi anthu omwe akuimila pachisankhochi za mfundo zachitukuko zomwe alonjeza kuzakwaniritsa atapambana pachisankho.

Izi zikuchitika panthawi yomwe bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC likuyembekezera kukhazikitsa nyengo yamisonkhano yokopa anthu pa 14 July ku Bingu international convention center mu dzinda wa Lilongwe.

Related posts

1 comment

Glory July 16, 2025 - 7:01 pm
Greater
Add Comment