Ngati njira imodzi yoonetsetsa kuti chitetezo ndi chokhwima kudera la Limbe, kampani ya Premier Bet lachisanu yapereka thandizo la ndalama zokwana 1 Million Kwacha komanso ma reflector okwana 100 a ndalama zokwana 1.3 million kwacha ku polisi ya  Limbe.

M’modzi mwa akuluakulu a kampani ya Premier Bet mumzinda wa Blantyre Hamza Mgaye wati kampaniyi yapereka thandizoli pozindikira ntchito yaikulu yomwe apolisi amagwira poteteza miyoyo komanso katundu wa mzika zadziko lino.

Poyankhula pamwambowu a Mgaye anati chitetezo ndi chothandizira kupititsa patsogolo ntchito zamalonda choncho ndikofunika kugwilira ntchito limodzi pakati pa nthambi zachitetezo ndi kampani zamalonda.

Iwo analonjeza kuti kampani ya premiere bet ipereka thandizo ndi kukonza katundu yemwe waonongeka kuphatikizapo galimoto pa polisi ya Limbe ndicholinga chochepetsetsa vuto la mayendedwe.

Polandira thandizoli mkulu wa polisi ya Limbe a Edwin Mnkhambo ayamikira kampani ya Premier bet kaamba kathandizoli lomwe lati lithandizira kuchepetsa ena mwa mavuto omwe polisiyi yakhala ikukumana nawo.

Amid Khan ndi wa pampando oyang’anira ubale pakati pa apolisi ndi anthu ozungulira polisi ya Limbe ndipo apempha kampani zina kuti zitengerepo phunziro pazomwe kampani ya Premiere Bet yachita popereka thandizoli.

Kupatula thandizoli polisi ya Limbe yadzala makanema achinsisi m’malo ozungulira derali zomwe zikuthandizira kuti ntchito yogwira anthu omwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi mchitidwe waumbava ndi umbanda ikhale yosavuta.

Related posts

Atsogoleri akhale patsogolo popeza mayankho othana ndi mavuto omwe akuta dziko lino-Sadana

Youths urged to be patriots of their communities